Miyambi 10:19-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Pocuruka mau zolakwa sizisoweka;Koma wokhala cete acita mwanzeru.

20. Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika;Koma mtima wa oipa uli wacabe.

21. Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri;Koma zitsiru zimafa posowa nzeru.

22. Madalitso a Yehova alemeretsa,Saonjezerapo cisoni.

23. Masewero a citsiru ndiwo kucita zoipa;Koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru.

Miyambi 10