Miyambi 10:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira;Koma wopusa pamsana pace ntyole.

14. Anzeru akundika zomwe adziwaKoma m'kamwa mwa citsiru muononga tsopano lino.

15. Cuma ca wolemera ndi mudzi wace wolimba;Koma umphawi wao uononga osauka.

16. Nchito za wolungama zipatsa moyo;Koma phindu la oipa licimwitsa.

17. Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo;Koma wosiya cidzudzulo asocera.

Miyambi 10