4. Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao.
5. Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.
6. Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amace, mpongozi aukira mpongozi wace; adani ace a munthu ndiwo a m'nyumba yace.
7. Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa cipulumutso canga; Mulungu wanga adzandimvera.
8. Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga.
9. Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, cifukwa ndamcimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditurutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya cilungamo cace.
10. Pamenepo mdani wanga adzaciona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.