1. Koma kudzacitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.
2. Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zace, ndipo tidzayenda m'mabande ace; pakuti ku Ziyoni kudzaturuka cilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.
3. Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzace lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.