Mika 1:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. MAU a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Morese masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.

2. Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse ziri m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m'Kacisi wace wopatulika.

3. Pakuti, taonani, Yehova alikuturuka m'malo mwace, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.

4. Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba.

Mika 1