15. Ndipo anamkhudza dzanja lace, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
16. Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo Iye anaturutsa mizimuyo ndi mau, naciritsa akudwala onse;
17. kotero kuti cikwaniridwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,Iye yekha anatenga zofoka zathu,Nanyamula nthenda zathu.
18. Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke ku tsidya lina,
19. Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kuli konse mumukako.
20. Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wace.
21. Ndipo wina wa ophunzira ace anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga.
22. Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao.
23. Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ace anamtsata Iye.
24. Ndipo onani, m panauka namondwe wamkuru panyanja, kotero kuti ngalawa inapfundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo.
25. Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tirikutayika.
26. Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikuru.
27. Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
28. Ndipo pofika Iye ku tsidya lina, ku dziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akuturuka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapa munthu pa njira imeneyo.
29. Ndipo onani, anapfuula nati, Tiri nanu ciani, inu Mwana wa Mulungu? mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yace siinafike?