1. Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.
2. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
3. Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?
4. Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli.
5. Wonyenga iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.