6. Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako, nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
7. Ndipo popemphera musabwereze-bwereze cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao.
8. Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.
9. Cifukwa cace pempherani inu comweci:Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
10. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano.
11. Mutipatse ife lero cakudya cathu calero.
12. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu.
13. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.
14. Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.
15. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.
16. Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
17. Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako:
18. kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.