24. Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.
25. Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?
26. Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
27. Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?