26. Indetu ndinena ndi iwe, sudzaturukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumariza ndiko.
27. Munamva kuti kunanenedwa, Usacite cigololo;
28. koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kucita naye cigololo mumtima mwace.
29. Koma 1 ngati diso lake lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'gehena.
30. Ndipo 2 ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losamuka thupi lako lonse kugehena.
31. Kunanenedwanso, Yense wakucotsa mkazi wace 3 ampatse iye cilekaniro:
32. koma Ine ndinena kwa inu, kuti 4 yense wakucotsa mkazi wace, kosati cifukwa ca cigololo, amcititsa cigololo: ndipo amene adzakwata wocotsedwayo acita cigololo.
33. Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, 5 Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako:
34. koma Ine ndinena kwa inu, 6 Musalumbire konse, kapena kuchula Kumwamba, cifukwa kuli cimpando ca Mulungu;
35. 7 kapena kuchula dziko lapansi, cifukwa liri popondapo mapazi ace; kapena kuchula Yerusalemu, cifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikurukuru.
36. 8 Kapena usalumbire ku mutu wako, cifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi.
37. 9 Kama manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo coonjezedwa pa izo cicokera kwa woipayo.
38. Munamva kuti kunanenedwa, 10 Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:
39. koma ndinena kwa inu, 11 Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako Lamanja, umtembenuzire linanso.
40. Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso copfunda cako.
41. Ndipo 12 amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.
42. Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye 13 wofuna kukukongola usampotolokere.
43. Munamva kuti kunanenedwa, 14 Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: