1. Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ace;
2. ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:
3. Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4. Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.
5. Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.
6. Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.
7. Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.
8. Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.