Mateyu 4:24-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo mbiri yace inabuka ku Suriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundu mitundu, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawaciritsa.

25. Ndipo inamtsata mipingo mipingo ya anthu ocokera ku Galileya, ndi ku Dekapole ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordano.

Mateyu 4