Mateyu 4:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pace anamva njala.

3. Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.

4. Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa,Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akuturuka m'kamwa mwa Mulungu.

Mateyu 4