Mateyu 27:54-66 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

54. Ndipo pamene mkuru wa asilikari, ndi iwo anali naye 11 akudikira Yesu, anaona cibvomezi, ndi zinthu zimene zinacitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyo ndiye Mwana wa Mulungu.

55. Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patari, 12 Omwe anatsata Yesu kucokera ku Galileya, namatumikira Iye;

56. mwa iwo 13 amene munali Mariya wa Magadala, ndi Mariya amace wa Yakobo, ndi wa Yose, ndi amace wa ana a Zebedayo.

57. Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wacuma wa ku Arimateya, dzina lace Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu;

58. yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe.

59. Ndipo Yosefe anatenga mtembo, naukulunga m'nsaru yabafuta yoyeretsa,

60. 14 nauika m'manda ace atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukuru pakhomo pa manda, nacokapo,

61. Ndipo Mariya wa Magadala anali pamenepo, ndi Mariya winayo, anakhala pansi popenyana ndi mandawoo

62. Ndipo m'mawa mwace, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe akuru ndi Afarisi anasonkhanira kwa Pilato,

63. nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, 15 Ndidzaukapofikamasikuatatu.

64. Cifukwa cace mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lacitatulo, kuti kapena ophunzira ace angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo cinyengo comariza cidzaposa coyambaco.

65. Pilato anati kwa iwo, Tengani alonda; mukani, kasungeni monga mudziwa.

66. Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, 16 nasindikizapo cizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.

Mateyu 27