30. Namthira malobvu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.
31. Ndipo pamene anatha kumcitira Iye cipongwe, anabvula malaya aja, nambveka Iye malaya ace, namtsogoza Iye kukampacika pamtanda.
32. Ndipo pakuturukapao anapeza munthu wa ku Kurene, dzina lace Simoni, namkangamiza iye kuti anyamule mtanda wace.
33. Ndipo pamene anadza kumalo dzina lace Golgota, ndiko kunena kuti, Malo-abade,
34. anamwetsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafuna kumwa.
35. Ndipo pamene anampacika Iye, anagawana zobvala zace ndi kulota maere:
36. nakhala iwo pansi, namdikira kumeneko.
37. Ndipo anaika pamwamba pamutu pace liwongo lace lolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA.
38. Pamenepo anapacika pamodzi ndi Iyeacifwamba awiri, mmodzi ku dzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.
39. Ndipo anthu akupitirirapo 1 anamcitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,
40. nati, Nanga 2 Iwe, wopasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; 3 ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo.
41. Comweconso ansembe akuru, pamodzi ndi alembi ndi akuru anamcitira cipongwe, nati,
42. Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye Mfumu ya Ayuda; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.
43. 4 Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.
44. Ndiponso 5 acifwambawo opacikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi.
45. Ndipo 6 ora lacisanu ndi cimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai.
46. Ndipo poyandikira ora lacisanu ndi cinai, Yesu 7 anapfuula ndi mau akuru, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
47. Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya.
48. Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, 8 natenga cinkhupule, nacidzaza ndi vinyo wosasa, naciika pabango, namwetsa Iye.
49. Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa.