Mateyu 27:26-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Pomwepo iye anamasulira iwo Baraba, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampacike pamtanda.

27. Pomwepo asilikari a kazembe anamuka naye Yesu ku bwalo la mirandu, nasonkhanitsa kwa iye khamu lao lonse.

28. Ndipo anabvula malaya ace, nambveka malaya ofiira acifumu.

29. Ndipo analuka korona waminga, nambveka pamutu pace, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lace; ndipo anagwada pansi pamaso pace, namcitira cipongwe, nati, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda!

30. Namthira malobvu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

Mateyu 27