Mateyu 27:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya,Monga anandilamulira ine Ambuye.

11. Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.

12. Ndipo pakumnenera Iye ansembe akuru ndi akuru, Iye sanayankha kanthu.

13. Pomwepo Pilato ananena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe?

14. Ndipo sanayankha Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu.

15. Ndipo pa Paskha kazembe adazolowera kumasulira anthu mmodzi wandende, amene iwo anafuna.

16. Ndipo pa nthawi yomweyo anali ndi wandende wodziwika, dzina lace Baraba.

17. Cifukwa cace pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Baraba kodi, kapena Yesu, wochedwa Kristu?

18. Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.

19. Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wace anatumiza mau kwa iye, kunena, Musacite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri cifukwa ca Iye.

Mateyu 27