1. Ndipo pakudza mamawa, ansembe akuru ndi akuru a anthu onse anakhala upo wakumcitira Yesu, kuti amuphe;
2. ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.
3. Pamenepo Yudase yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe akuru ndi akuru,
4. nanena, Ndinacita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tiri naco ciani ife? udzionere wekha.
5. Ndipo iye anataya pansi ndalamazo paKacisi, nacokapo, nadzipacika yekha pakhosi.
6. Ndipo ansembe akuru anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'cosonkhera ndalama za Mulungu, cifukwa ndizo mtengo wa mwazi.
7. Koma anapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda a alendo.
8. Cifukwa cace munda umenewu anaucha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino.