Mateyu 26:41-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka.

42. Anamukanso kaciwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ici sicingandipitirire, koma ndimwere ici, kufuna kwanu kucitidwe.

43. Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo.

44. Ndipo anawasiyanso, napemphera kacitatu, nateronso mau omwewo.

45. Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa munthu aperekedwa m'manja ocimwa.

46. Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira.

47. Ndipo Iye ali cilankhulire, onani, Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikuru la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kucokera kwa ansembe akuru ndi akuru a anthu.

48. Koma wompereka Iye anawapatsa cizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye.

49. Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa.

50. Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji: iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.

51. Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lace, nasolola Iupanga lace, nakantha kapolo wa mkuru wa ansembe, nadula khutu lace.

52. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza Iupanga lako m'cimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi Iupanga,

Mateyu 26