1. Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, naturuka kukakomana ndi mkwati.
2. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ocenjera.
3. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta;
4. koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.
5. Ndipo pamene mkwati anacedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.
6. Koma pakati pa usiku panali kupfuula, Onani, mkwati! turukani kukakomana naye.