Mateyu 25:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, naturuka kukakomana ndi mkwati.

2. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ocenjera.

3. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta;

4. koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao.

Mateyu 25