5. Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Kristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.
6. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma citsiriziro sicinafike.
7. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zibvomezi m'malo akuti akuti.
8. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.
9. Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, cifukwa ca dzina langa.
10. Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzace, nadzadana wina ndi mnzace.
11. Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsaanthuambiri.
12. Ndipo cifukwa ca kucuruka kwa kusayeruzika, cikondano ca anthu aunyinji cidzazirala.
13. Koma iye wakulimbika cilimbikire kufikira kucimariziro, yemweyo adzapulumuka.
14. Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu h mitundu yonse; ndipo pomwepo cidzafika cimariziro.
15. Cifukwa cace m'mene mukadzaona conyansa ca kupululutsa, cimene cidanenedwa ndi Danieli mneneri, citaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
16. pomwepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri:
17. iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwace;