Mateyu 24:45-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

45. 6 Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wace anamkhazika woyang'anira banja lace, kuwapatsa zakudya pa nthawi yace?

46. Wodala kapolo amene mbuye wace, pakufika, adzampeza iye alikucita cotero.

47. Indetu, ndinena kwa inu, kuti 7 adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zace zonse.

48. Koma kapolo woipa akanena mumtima mwace, Mbuye wanga wacedwa;

Mateyu 24