30. ndi kuti, Ife tikadakhala m'masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri.
31. Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.
32. Dzazani inu muyeso wa makolo anu.
33. Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwace kwa gehena?