28. Comweco inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi cinyengo ndi kusayeruzika.
29. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama,
30. ndi kuti, Ife tikadakhala m'masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri.
31. Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri.
32. Dzazani inu muyeso wa makolo anu.