2. Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wace phwando la ukwati,
3. natumiza akapolo ace kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.
4. Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsya: idzani kuukwati.
5. Koma iwo ananyalanyaza, nacoka, wina ku munda wace, wina ku malonda ace:
6. ndipo otsala anagwira akapolo ace, nawacitira cipongwe, nawapha.
7. Koma mfumu inakwiya; nituma asilikari ace napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.
8. Pomwepo inanena kwa akapolo ace, Za ukwati tsopano zapsya, koma oitanidwawo sanayenera.
9. Cifukwa cace pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene ali yense mukampeze, itanani kuukwatiku.
10. Ndipo akapolo ao anaturukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pacakudya.
11. Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosabvala cobvala ca ukwati;
12. nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala naco cobvala ca ukwati? Ndipo iye analibe mau.
13. Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye ku mdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
14. Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka.
15. Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwace.