Mateyu 22:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yesn anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati,

2. Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wace phwando la ukwati,

3. natumiza akapolo ace kukaitana oitanidwa ku ukwati umene; ndipo iwo sanafuna kudza.

4. Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsya: idzani kuukwati.

5. Koma iwo ananyalanyaza, nacoka, wina ku munda wace, wina ku malonda ace:

6. ndipo otsala anagwira akapolo ace, nawacitira cipongwe, nawapha.

7. Koma mfumu inakwiya; nituma asilikari ace napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao.

8. Pomwepo inanena kwa akapolo ace, Za ukwati tsopano zapsya, koma oitanidwawo sanayenera.

9. Cifukwa cace pitani inu ku mphambano za njira, ndipo amene ali yense mukampeze, itanani kuukwatiku.

Mateyu 22