11. Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,
12. nati, Omarizira awa anagwira nchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi: kutentha kwace.
13. Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi?