Mateyu 20:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anaturuka mamawa kuka lembera anchito a m'munda wace wampesa.

2. Ndipo parnene adapangana ndi anchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza ku munda wace.

3. Ndipo anaturuka dzuwa litakwera, naona ena ataima cabe pabwalo;

4. ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani cimene ciri coyenera. Ndipo iwo anapita.

5. Ndiponso anaturuka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nacita cimodzimodzi.

6. Ndipo poyandikira madzulo anaturuka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse cabe?

7. Iwo ananena kwa iye, Cifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso ku mundawo wampesa.

8. Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wace, Kaitane anchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omarizira kufikira kwa oyamba.

9. Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu ali yense rupiya latheka limodzi.

10. Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka.

11. Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,

12. nati, Omarizira awa anagwira nchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi: kutentha kwace.

Mateyu 20