Mateyu 17:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wace, napita nao pa okha pa phiri lalitari;

2. ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yace inawala monga dzuwa, ndi zobvala zace zinakhala zoyera mbu monga kuwala.

3. Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi Iye.

Mateyu 17