Mateyu 16:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Obadwa oipa ndi acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sadzalandira cizindikiro cina, koma cizindikiro ca Yona. Ndipo Iye anawasiya, nacokapo.

5. Ndipo ophunzira anadza ku tsidya linalo, naiwala kutenga mikate.

6. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe cotupitsa mkate ca Afarisi ndi Asaduki.

7. Ndipo iwo anafunsana wina ndi mnzace, nati, Sitinatenga mikate.

8. Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana cifukwa ninji wina ndi mnzace, kuti simunatenga mikate?

9. kodi cikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi mitanga ingati munaitola?

10. Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi malicero angati munawatola?

11. Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani cotupitsa ca Afarisi ndi Asaduki.

12. Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauza kupewa cotupitsa ca mikate, koma ciphunzitso ca Afarisi ndi Asaduki.

13. Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kaisareya wa Filipi, anafunsa ophunzira ace, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye yani?

14. Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.

15. Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani?

16. Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.

Mateyu 16