Mateyu 16:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo.

19. Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo cimene ukamanga pa dziko lapansi cidzakhala comangidwa Kumwamba: ndipo cimene ukacimasula pa dziko lapansi, cidzakhala comasulidwa Kumwamba.

20. Pamenepo analamulira ophunzira kuti asauze munthu kuti Iye ndiye Kristu.

Mateyu 16