Mateyu 15:12-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva conenaco?

13. Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzala, udzazulidwa.

14. Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.

15. Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli.

16. Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala cipulukirire?

17. Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo?

18. Koma zakuturuka m'kamwa zicokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu.

19. Pakuti mumtima mucokera maganizo oipa, zakupha, zacigololo, zaciwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;

20. izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthuai.

21. Ndipo Yesu anaturukapo napatukira ku mbali za Turo ndi Sidoni.

22. Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anaturuka m'malire, napfuula, nati, Mundicitire ine cifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi ciwanda.

23. Koma Iye sanamyankha mau amodzi. Ndipo ophunzira ace anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti apfuula pambuyo pathu.

24. Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israyeli.

25. Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine.

26. Ndipo Iye anayankha, nati, Sicabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagaru.

Mateyu 15