Mateyu 14:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, mitanga khumi ndi iwiri yodzala.

21. Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana.

22. Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye ku tsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke.

23. Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.

24. Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao.

25. Ndipo pa ulonda wacinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja.

26. Koma m'mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, ndi mzukwa! Ndipo anapfuula ndi mantha.

27. Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope.

28. Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa lou pamadzi.

29. Ndipo Iye anati, Idza, Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.

30. Koma m'mene iye anaiona mphepo, ana, opa; ndipo poyamba kunura, anapfuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine!

31. Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lace, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?

Mateyu 14