1. Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu,
2. nanena kwa anyamata ace, U yo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo cifukwa ca ici zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.
3. Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende cifukwa ca Herodiya, mkazi wa mbale wace Filipo.
4. Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye.
5. Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri.
6. Koma pakufika tsiku la kubadwa kwace kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya anabvina pakati pao, namkondweretsa Herode.
7. Pomwepo iye anamlonjeza cilumbirire, kumpatsa iye cimene ciri conse akapempha.
8. Ndipo iye, atampangira amace, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbizi mutu wa Yohane Mbatizi. Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi cisoni;
9. koma cifukwa ca malumbiro ace, ndi ca iwo anali naye pacakudya, analamulira upatsidwe;
10. ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende.
11. Ndipo anautenga mutu wace m'mbizimo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amace.
12. Ndipo ophunzira ace anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu.
13. Ndipo Yesu pakumva, anacokera kumeneko m'ngalawa, kunka ku malo acipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kucokera m'midzi.
14. Ndipo Iye anaturuka, naona khamu lalikuru la anthu, nacitira iwo cifundo, naciritsa akudwala ao.