19. Sadzalimbana, sadzapfuula;Ngakhale mmodzi sadzamva mau ace m'makwalala;
20. Bango lophwanyika sadzalityola,Ndi nyali yofuka sadzaizima,Kufikira Iye adzatumiza ciweruzo cikagonjetse,
21. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lace.
22. Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi ciwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamciritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.
23. Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?