Mateyu 12:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuiturutsa?

12. Nanga kuposa kwace kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Cifukwa ca ici nkuloleka kucita zabwino tsiku la Sabata.

13. Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja Lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzace.

14. Ndipo Afarisi anaturuka, nakhala upo womcitira Iye mwa kumuononga.

Mateyu 12