Masalmo 92:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ha! nchito zanu nzazikuru, Yehova,Zolingalira zanu nzozama ndithu.

6. Munthu wopulukira sacidziwa;Ndi munthu wopusa sacizindikira ici;

7. Cakuti pophuka oipa ngati msipu,Ndi popindula ocita zopanda pace;Citero kuti adzaonongeke kosatha:

8. Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba ku nthawi yonse.

9. Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,Pakuti, taonani, adani anu adzatayika;Ocita zopanda pace onse adzamwazika.

Masalmo 92