Masalmo 90:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamoM'mibadwo mibadwo.

2. Asanabadwe mapiri,Kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu,Inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha,Inu ndinu Mulungu.

3. Mubweza munthu akhale pfumbi;Nimuti, Bwererani inu, ana a anthu.

4. Pakuti pamaso panu zaka zikwiZikhala ngati dzulo, litapita,Ndi monga ulonda wa usiku.

Masalmo 90