Masalmo 40:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,Zocimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;Ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandicokera mtima.

13. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni:Fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

14. Acite manyazi nadodomeIwo akulondola moyo wanga kuti auononge:Abwerere m'mbuyo, nacite manyazi iwo okondwera kundicitira coipa.

15. Apululuke, mobwezera manyazi aoAmene anena nane, Hede, hede.

Masalmo 40