Masalmo 37:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ambuye adzamseka:Popeza apenya kuti tsiku lace likudza.

14. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;Alikhe ozunzika ndi aumphawi,Aphe amene ali oongoka m'njira:

15. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe,Ndipo mauta ao adzatyoledwa.

16. Zocepa zace za wolungama zikomaKoposa kucuruka kwao kwa oipa ambiri.

17. Pakuti manja a oipa adzatyoledwa:Koma Yehova acirikiza olungama.

Masalmo 37