Masalmo 32:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Musakhale monga kavalo, kapena ngati buru, wopanda nzeru:Zomangira zao ndizo cam'kamwa ndi capamutu zakuwakokera,Pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.

10. Zisoni zambiri zigwera woipa:Koma cifundo cidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.

11. Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima;Ndipo pfuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.

Masalmo 32