Masalmo 3:5-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;Ndinauka; pakuti Yehova anandicirikiza.

6. Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.

7. Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;Mwawatyola mano oipawo.

8. Cipulumutso nca Yehova;Dalitso lanu likhale pa anthu anu.

Masalmo 3