Masalmo 25:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Musakumbukile zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu:Mundikumbukile monga mwa cifundo canu,Cifukwa ca ubwino wanu, Yehova.

8. Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima:Cifukwa cace adzaphunzitsa olawa za njira.

9. Adzawatsogolera ofatsa m'ciweruzo:Ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yace.

10. Mayendedwe onse a Yehova ndiwo cifundo ndi coonadi,Kwa iwo akusunga pangano lace ndi mboni zace.

11. Cifukwa ca dzina lanu, Yehova,Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru.

Masalmo 25