Masalmo 25:5-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Munditsogolere m'coonadi canu, ndipo mundiphunzitse;Pakuti Inu ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

6. Kumbukilani, Yehova, nsoni zanu ndi cifundo canu;Pakuti izi nza kale lonse,

7. Musakumbukile zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu:Mundikumbukile monga mwa cifundo canu,Cifukwa ca ubwino wanu, Yehova.

Masalmo 25