Masalmo 22:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai:Cotonza ca anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.

7. Onse akundipenya andiseka:Akwenzula, apukusa mutu, nati,

8. Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa,Amlanditse tsopano popeza akondwera naye.

9. Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa:Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.

10. Cibadwire ine anandisiyira Inu:Kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu.

11. Musandikhalire kutali; pakuti nsautso iri pafupi:Pakuti palibe mthandizi.

12. Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga:Mphongo zolimba za ku Basana zandizungulira,

Masalmo 22