Masalmo 18:6-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova,Ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;Mau anga anawamva m'Kacisi mwace,Ndipo mkuwo wanga wa pankhope pace unalowa m'makutu mwace.

7. Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi.Ndi maziko a mapiri ananjenjemeraNagwedezeka, pakuti anakwiya iyeyo.

8. Unakwera utsi woturuka m'mphuno mwace:Ndi moto wa m'kamwa mwace unanyeka:Nuyakitsa makara.

9. Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;Ndipo pansi pa mapazi ace panali mdima bii.

10. Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka;Nauluka msanga pa mapiko a mphepo,

11. Anaika mdima pobisala pace, hema wace womzinga;Mdima wa madzi, makongwa a kuthambo.

12. Mwa kucezemira kunali pamaso pace makongwa anakanganuka,Matalala ndi makala amoto.

13. Ndipo anagunda m'mwamba Yehova,Ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lace;Matalala ndi makala amoto,

14. Ndipo anatuma mibvi yace nawabalalitsa;Inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

15. Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi,Nafukuka maziko a dziko lapansi,Mwa kudzudzula kwanu, Yehova,Mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.

16. Anatuma kucokera m'mwamba, ananditenga;Anandibvuula m'madzi ambiri.

17. Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu,Ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

18. Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga.

19. Ananditurutsanso andifikitse motakasuka;Anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20. Yehova anandibwezera monga mwa cilungamo canga;Anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21. Pakuti ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinacitira coipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

Masalmo 18