15. Ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu,Ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yace,Ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.
16. Mitengo ya Mulungu yadzala ndi madzi;Mikungudza ya ku Lebano imene anaioka;
17. M'mwemo mbalame zimanga zisa zao;Pokhala cumba mpa mitengo ya mikungudza,
18. Mapiri atali ndiwo ayenera zinkhoma;Pamatanthwe mpothawirapo mbira.
19. Anaika mwezi nyengo zace;Dzuwa lidziwa polowera pace.
20. Muika mdima ndipo pali usiku;Pamenepo zituruka zirombo zonse za m'thengo.
21. Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao,Nifuna cakudya cao kwa Mulungu.
22. Poturuka dzuwa, zithawa, Zigona pansi m'ngaka mwao.
23. Pamenepo munthu aturukira ku nchito yace,Nagwiritsa kufikira madzulo.
24. Nchito zanu zicurukadi, Yehova!Munazicita zonse mwanzeru;Dziko lapansi lidzala naco cuma canu.
25. Nyanja siyo, yaikuru ndi yacitando,M'mwemo muli zokwawa zosawerengeka;Zamoyo zazing'ono ndi zazikuru.
26. M'mwemo muyenda zombo;Ndi livyatanu amene munamlenga aseweremo.
27. Izi zonse zikulindirirani,Muzipatse cakudya cao pa nyengo yace.
28. Cimene muzipatsa zigwira;Mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino.
29. Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa;Mukalanda mpweya wao, zikufa,Nizibwerera kupfumbi kwao.
30. Potumizira mzimu wanu, zilengedwa;Ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.
31. Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha;Yehova akondwere mu nchito zace;
32. Amene apenyerera pa dziko lapansi, ndipo linjenjemera;Akhudza mapiri, ndipo afuka.
33. Ndidzayimbira Yehova m'moyo mwanga:Ndidzayimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndiripo.