Masalmo 103:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Monga atate acitira ana ace cifundo,Yehova acitira cifundo iwo akumuopa Iye.

14. Popeza adziwa mapangidwe athu;Akumbukila kuti ife ndife pfumbi.

15. Koma munthu, masiku ace akunga udzu;Aphuka monga duwa la kuthengo.

16. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe:Ndi malo ace salidziwanso.

17. Koma cifundo ca Yehova ndico coyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye,Ndi cilungamo cace kufikira kwa ana a ana;

Masalmo 103