Marko 8:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikuru la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, iye anadziitanira ophunzira ace, nanena nao,

2. Ndimva nalo cifundo khamulo, cifukwa ali ndi Ine cikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya:

3. ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena iwo acokera kutali.

4. Ndipo ophunzira ace anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m'cipululu muno?

Marko 8